Yamikani Yehova ndi kuthira mang'ombe; muimbireni Mulungu wathu zomlemekeza pazeze:
Imbirani Chauta mothokoza, imbirani Mulungu wathu nyimbo yokoma ndi pangwe.
Imbirani Yehova ndi mayamiko; imbani nyimbo kwa Mulungu ndi pangwe.
Imbirani Mulungu, maufumu a dziko lapansi inu; imbirani Ambuye zomlemekeza.
Muimbireni Yehova zomlemekeza ndi zeze; ndi zeze ndi mau a salimo.