Ndipo anamtulutsa iye kunja, nati, Tayang'anatu kumwamba, uwerenge nyenyezi, ngati ukhoza kuziwerenga zimenezo: ndipo anati kwa iye, Zoterezo zidzakhala mbeu zako.
Masalimo 147:4 - Buku Lopatulika Awerenga nyenyezi momwe zili; azitcha maina zonsezi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Awerenga nyenyezi momwe zili; azitcha maina zonsezi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Amadziŵa chiŵerengero cha nyenyezi, zonse amazitcha maina ake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Amadziwa chiwerengero cha nyenyezi, ndipo iliyonse amayitchula dzina. |
Ndipo anamtulutsa iye kunja, nati, Tayang'anatu kumwamba, uwerenge nyenyezi, ngati ukhoza kuziwerenga zimenezo: ndipo anati kwa iye, Zoterezo zidzakhala mbeu zako.
Pakuona ine thambo la kumwamba lanu, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi, zimene munazikhazika,
Kwezani maso anu kumwamba, muone amene analenga izo, amene atulutsa khamu lao ndi kuziwerenga; azitcha zonse maina ao, ndi mphamvu zake zazikulu, ndi popeza ali wolimba mphamvu, palibe imodzi isoweka.