Masalimo 147:12 - Buku Lopatulika Yerusalemu, lemekezani Yehova; Ziyoni, lemekezani Mulungu wanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yerusalemu, lemekezani Yehova; Ziyoni, lemekezani Mulungu wanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tamanda Chauta, iwe Yerusalemu. Tamanda Mulungu wako, iwe Ziyoni. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Lemekeza Yehova, iwe Yerusalemu; tamanda Mulungu wako, iwe Ziyoni, |
Tafuula, takuwa iwe, wokhala mu Ziyoni, chifukwa Woyera wa Israele wa m'kati mwako ali wamkulu.
Ha, akongolatu pamapiri mapazi a iye amene adza ndi uthenga wabwino, amene abukitsa mtendere, amene adza ndi uthenga wabwino wa zinthu zabwino, amene abukitsa chipulumutso; amene ati kwa Ziyoni, Mulungu wako ndi mfumu.
Mukondwere tsono, inu ana a Ziyoni, nimusekerere mu Yehova Mulungu wanu; pakuti adzayamba kukupatsani mvula ya chizimalupsa, monga mwa chilungamo chake; nakuvumbitsirani mvula, mvula ya chizimalupsa ndi ya masika mwezi woyamba.