Koma ansembe ambiri, ndi Alevi, ndi akulu a nyumba za makolo, okalamba amene adaona nyumba yoyamba ija, pomanga maziko a nyumba iyi pamaso pao, analira ndi mau aakulu; koma ambiri anafuulitsa mokondwera.
Masalimo 147:1 - Buku Lopatulika Aleluya; Pakuti kuimbira zomlemekeza Mulungu wathu nkokoma; pakuti chikondweretsa ichi, chilemekezo chiyenera. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Aleluya; Pakuti kuimbira zomlemekeza Mulungu wathu nkokoma; pakuti chikondwetsa ichi, chilemekezo chiyenera. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tamandani Chauta! Nkwabwino kuimba nyimbo zotamanda Mulungu wathu, nkokondwetsa mtima kumtamanda moyenera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tamandani Yehova. Nʼkwabwino kwambiri kuyimba nyimbo zamatamando kwa Mulungu wathu, nʼkokondweretsa ndi koyenera kumutamanda! |
Koma ansembe ambiri, ndi Alevi, ndi akulu a nyumba za makolo, okalamba amene adaona nyumba yoyamba ija, pomanga maziko a nyumba iyi pamaso pao, analira ndi mau aakulu; koma ambiri anafuulitsa mokondwera.
Lemekezani Yehova; pakuti Yehova ndiye wabwino; muimbire zolemekeza dzina lake; pakuti nkokondweretsa kutero.
Ndidzikumbukira izi ndipo nditsanulira moyo wanga m'kati mwa ine, pakuti ndinkapita ndi unyinji wa anthu, ndinawatsogolera kunyumba ya Mulungu, ndi mau akuimbitsa ndi kuyamika, ndi unyinji wakusunga dzuwa lokondwera.