Ndipo Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m'mphuno mwake; munthuyo nakhala wamoyo.
Masalimo 146:4 - Buku Lopatulika Mpweya wake uchoka, abwerera kunka kunthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mpweya wake uchoka, abwerera kunka kunthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene mpweya wa munthu uchokeratu, munthuyo amabwerera ku dothi, zimene ankafuna kuchita, zimatha tsiku lomwelo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene mizimu yawo yachoka, iwo amabwerera ku dothi; zimene ankafuna kuchita zimatha tsiku lomwelo. |
Ndipo Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m'mphuno mwake; munthuyo nakhala wamoyo.
m'thukuta la nkhope yako udzadya chakudya, kufikira kuti udzabwerera kunthaka: chifukwa kuti m'menemo unatengedwa: chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.
Ndine, taonani, ndipo Ine ndidzadzetsa chigumula cha madzi padziko lapansi, kuti chiononge zamoyo zonse, m'mene muli mpweya wa moyo pansi pathambo; zinthu zonse za m'dziko lapansi zidzafa.
Mukabisa nkhope yanu, ziopsedwa; mukalanda mpweya wao, zikufa, ndipo zibwerera kufumbi kwao.
fumbi ndi kubwera pansi pomwe linali kale, mzimu ndi kubwera kwa Mulungu amene anaupereka.
Chikondi chao ndi mdano wao ndi dumbo lao lomwe zatha tsopano; ndipo nthawi yamuyaya sagawa konse kanthu kalikonse kachitidwe pansi pano.
Siyani munthu, amene mpweya wake uli m'mphuno mwake; chifukwa m'mene awerengedwamo ndi muti?
Wodzozedwa wa Yehova, ndiye mpweya wa m'mphuno mwathu, anagwidwa m'maenje ao; amene tinanena kuti, Tidzakhala m'mthunzi mwake pakati pa amitundu,
koma munadzikweza kutsutsana naye Ambuye wa Kumwamba; ndipo anabwera nazo zotengera za nyumba yake kwa inu; ndi inu ndi akulu anu, akazi anu ndi akazi anu aang'ono, mwamweramo vinyo; mwalemekezanso milungu yasiliva, ndi yagolide, yamkuwa, yachitsulo, yamtengo, ndi yamwala, imene siiona kapena kumva, kapena kudziwa; ndi Mulungu amene m'dzanja mwake muli mpweya wanu, ndi njira zanu zonse, yemweyo simunamchitire ulemu.
Koma tilankhula nzeru mwa angwiro; koma si nzeru ya nthawi ino ya pansi pano, kapena ya akulu a nthawi ino ya pansi pano, amene alinkuthedwa;