Masalimo 146:10 - Buku Lopatulika Yehova adzachita ufumu kosatha, Mulungu wako, Ziyoni, ku mibadwomibadwo. Aleluya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yehova adzachita ufumu kosatha, Mulungu wako, Ziyoni, ku mibadwomibadwo. Aleluya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta adzakhala mfumu mpaka muyaya, Mulungu wako, iwe Ziyoni, adzalamulira ku mibadwo yonse. Tamandani Chauta! Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova ndiye Mfumu mpaka muyaya, Mulungu wako iwe Ziyoni, pa mibado yonse. Tamandani Yehova. |
Tafuula, takuwa iwe, wokhala mu Ziyoni, chifukwa Woyera wa Israele wa m'kati mwako ali wamkulu.
Iwe amene utengera mau abwino ku Ziyoni, kwera iwe pamwamba paphiri lalitali; iwe amene utengera mau abwino ku Yerusalemu, kweza mau ako ndi mphamvu, kwezetsa usaope, nena kumizinda ya Yuda, Taonani, Mulungu wanu!
Ha, akongolatu pamapiri mapazi a iye amene adza ndi uthenga wabwino, amene abukitsa mtendere, amene adza ndi uthenga wabwino wa zinthu zabwino, amene abukitsa chipulumutso; amene ati kwa Ziyoni, Mulungu wako ndi mfumu.
Za kuwonjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha pa mpando wachifumu wa Davide, ndi pa ufumu wake, kuukhazikitsa, ndi kuuchirikiza ndi chiweruziro ndi chilungamo kuyambira tsopano ndi kunkabe nthawi zonse. Changu cha Yehova wa makamu chidzachita zimenezi.
Ndipo masiku a mafumu aja Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzaonongeka kunthawi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu ao onse, nudzakhala chikhalire.
Ndilamulira ine kuti m'maiko onse a ufumu wanga anthu anjenjemere, naope pamaso pa Mulungu wa Daniele; pakuti Iye ndiye Mulungu wamoyo wakukhala chikhalire, ndi ufumu wake ngwosaonongeka, ndi kulamulira kwake kudzakhala mpaka chimaliziro.
Ndipo anampatsa ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu, kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe onse, amtumikire; ulamuliro wake ndi ulamuliro wosatha wosapitirira, ndi ufumu wake sudzaonongeka.
Momwemo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu wakukhala mu Ziyoni, phiri langa lopatulika; pamenepo Yerusalemu adzakhala wopatulika, osapitanso alendo pakati pake,
Ndipo mngelo wachisanu ndi chiwiri anaomba lipenga, ndipo panakhala mau aakulu mu Mwamba, ndi kunena, Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu, ndi wa Khristu wake: ndipo adzachita ufumu kufikira nthawi za nthawi.