Tanimphitsani chifundo chanu pa iwo akudziwa Inu; ndi chilungamo chanu pa oongoka mtima.
Masalimo 145:7 - Buku Lopatulika Adzabukitsa chikumbukiro cha ubwino wanu waukulu, nadzaimbira chilungamo chanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Adzabukitsa chikumbukiro cha ubwino wanu waukulu, nadzaimbira chilungamo chanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adzasimba za ubwino wanu, adzaimba nyimbo zotamanda kulungama kwanu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Adzakondwerera kuchuluka kwa ubwino wanu, ndi kuyimba mwachimwemwe za chilungamo chanu. |
Tanimphitsani chifundo chanu pa iwo akudziwa Inu; ndi chilungamo chanu pa oongoka mtima.
Mundilanditse kumlandu wa mwazi, Mulungu, ndinu Mulungu wa chipulumutso changa; lilime langa lidzakweza nyimbo ya chilungamo chanu.
Chilungamo chanunso, Mulungu, chifikira kuthambo; Inu amene munachita zazikulu, akunga Inu ndani, Mulungu?
Ndidzatchula zachifundo chake cha Yehova, ndi matamando a Yehova, monga mwa zonse zimene Yehova wapereka kwa ife; ndi ubwino wake waukulu kwa banja la Israele, umene Iye wapereka kwa iwo, monga mwa chifundo chake, ndi monga mwa ntchito zochuluka za chikondi chake.
Masiku ake Yuda adzapulumutsidwa, ndipo Israele adzakhala mokhazikika, dzina lake adzatchedwa nalo, ndilo Yehova ndiye chilungamo chathu.