Ndipo Isaki anatuluka kulingalira m'munda madzulo; ndipo anatukula maso ake, nayang'ana, taona, ngamira zinalinkudza.
Masalimo 145:5 - Buku Lopatulika Ndidzalingalira ulemerero waukulu wa ulemu wanu, ndi ntchito zanu zodabwitsa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndidzalingalira ulemerero waukulu wa ulemu wanu, ndi ntchito zanu zodabwitsa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndidzasinkhasinkha za ulemerero ndi za ufumu wanu waukulu, ndidzalingalira za ntchito zanu zodabwitsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Adzayankhula ulemerero wokongola waufumu wanu, ndipo ine ndidzalingalira za ntchito zanu zodabwitsa. |
Ndipo Isaki anatuluka kulingalira m'munda madzulo; ndipo anatukula maso ake, nayang'ana, taona, ngamira zinalinkudza.
Lilime langa lomwe lidzalankhula za chilungamo chanu tsiku lonse, pakuti ofuna kundichitira choipa achita manyazi, nadodoma.
Tsiku lomwelo mudzati, Muyamikire Yehova, bukitsani dzina lake, mulalikire machitidwe ake mwa mitundu ya anthu, munene kuti dzina lake lakwezedwa.
Tsono ine Nebukadinezara ndiyamika, ndi kukuza, ndi kulemekeza Mfumu ya Kumwamba, pakuti ntchito zake zonse nzoona, ndi njira zake chiweruzo; ndi oyenda m'kudzikuza kwao, Iye akhoza kuwachepetsa.