Pakuti Yehova ali wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu; ayenera amuope koposa milungu yonse.
Masalimo 145:3 - Buku Lopatulika Yehova ndi wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu; ndi ukulu wake ngwosasanthulika. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yehova ndi wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu; ndi ukulu wake ngwosasanthulika. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta ndi wamkulu ndi woyenera kumtamanda kwambiri, ndipo ukulu wake sitingathe kuumvetsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova ndi wamkulu ndi woyenera matamando onse; ukulu wake palibe angawumvetsetse. |
Pakuti Yehova ali wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu; ayenera amuope koposa milungu yonse.
Taonani, awa ndi malekezero a njira zake; ndi chimene tikumva za Iye ndi chinong'onezo chaching'ono; koma kugunda kwa mphamvu yake akuzindikiritsa ndani?
Taonani, Mulungu ndiye wamkulu, ndipo sitimdziwa; chiwerengo cha zaka zake nchosasanthulika.
Kunena za Wamphamvuyonse, sitingamsanthule; ndiye wa mphamvu yoposa; koma mwa chiweruzo ndi chilungamo chochuluka samasautsa.
Yehova ndiye wamkulu, ayenera kulemekezekadi, m'mzinda wa Mulungu wathu, m'phiri lake loyera.
Pakuti Yehova ndi wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu; ayenera amuope koposa milungu yonse.
Kodi iwe sunadziwe? Kodi sunamve? Mulungu wachikhalire, Yehova, Mlengi wa malekezero a dziko lapansi, salefuka konse, salema; nzeru zake sizisanthulika.
Ha! Kuya kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziwa kwake kwa Mulungu! Osasanthulikadi maweruzo ake, ndi njira zake nzosalondoleka!
Ndipo aimba nyimbo ya Mose kapolo wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa, nanena, Ntchito zanu nzazikulu ndi zozizwitsa, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse; njira zanu nzolungama ndi zoona, Mfumu Inu ya nthawi zosatha.