Ndipo anasiyako ku likasa la chipangano la Yehova Asafu ndi abale ake, atumikire kulikasa kosalekeza, monga umo mudzafunika tsiku ndi tsiku;
Masalimo 145:2 - Buku Lopatulika Masiku onse ndidzakuyamikani; ndi kulemekeza dzina lanu kunthawi za nthawi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Masiku onse ndidzakuyamikani; ndi kulemekeza dzina lanu kunthawi za nthawi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndidzakuthokozani tsiku ndi tsiku, ndidzatamanda dzina lanu mpaka muyaya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndidzakutamandani tsiku ndi tsiku ndi kulemekeza dzina lanu ku nthawi za nthawi. |
Ndipo anasiyako ku likasa la chipangano la Yehova Asafu ndi abale ake, atumikire kulikasa kosalekeza, monga umo mudzafunika tsiku ndi tsiku;
Ndidzalemekeza Yehova m'moyo mwanga; ndidzaimbira zomlemekeza Mulungu wanga pokhala ndi moyo ine.
Inu munandigwiriziza kuyambira ndisanabadwe, kuyambira pa thupi la mai wanga wondichitira zokoma ndinu; ndidzakulemekezani kosalekeza.
Ndipo iye adzakhala ndi moyo; ndipo adzampatsa golide wa ku Sheba; nadzampempherera kosalekeza; adzamlemekeza tsiku lonse.
Muimbireni Yehova, lemekezani dzina lake; lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.
Chifukwa chake ali kumpando wachifumu wa Mulungu; ndipo amtumikira Iye usana ndi usiku mu Kachisi mwake; ndipo Iye wakukhala pa mpando wachifumu adzawachitira mthunzi,