Masalimo 144:1 - Buku Lopatulika Wolemekezeka Yehova thanthwe langa, wakuphunzitsa manja anga achite nkhondo, zala zanga zigwirane nao: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Wolemekezeka Yehova thanthwe langa, wakuphunzitsa manja anga achite nkhondo, zala zanga zigwirane nao: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Atamandike Chauta, thanthwe langa londitchinjiriza, amene amaphunzitsa manja anga ndi zala zanga kumenya nkhondo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atamandike Yehova Thanthwe langa, amene amaphunzitsa manja anga kuchita nkhondo; zala zanga kumenya nkhondo. |
Nati kwa mfumu ya Israele, Pingiridzani. Napingiridza. Ndipo Elisa anasanjika manja ake pa manja a mfumu.
Yehova ndiye thanthwe langa, ndi linga langa, ndi Mpulumutsi wanga; Mulungu wanga, ngaka yanga, ndidzakhulupirira Iye; chikopa changa, nyanga ya chipulumutso changa, msanje wanga.
Ndipo mwandipatsa chikopa cha chipulumutso chanu; ndipo dzanja lamanja lanu landigwiriziza, ndipo chifatso chanu chandikuza ine.
Mundikhalire thanthwe lokhalamo, lopitako kosaleka; mwalamulira kundipulumutsa; popeza Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa.
Khulupirirani Yehova nthawi zamuyaya, pakuti mwa Ambuye Yehova muli thanthwe lachikhalire.
Koma mwa Yehova yekha, wina adzati kwa Ine, muli chilungamo ndi mphamvu; ngakhale kwa Iyeyo anthu adzafika, ndi onse amene anamkwiyira, adzakhala ndi manyazi.
(pakuti zida za nkhondo yathu sizili za thupi, koma zamphamvu mwa Mulungu zakupasula malinga);