Mundizindikiritse, ndipo ndidzasunga malamulo anu; ndidzawasamalira ndi mtima wanga wonse.
Masalimo 143:8 - Buku Lopatulika Mundimvetse chifundo chanu mamawa; popeza ndikhulupirira Inu: Mundidziwitse njira ndiyendemo; popeza ndikweza moyo wanga kwa Inu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mundimvetse chifundo chanu mamawa; popeza ndikhulupirira Inu: Mundidziwitse njira ndiyendemo; popeza ndikweza moyo wanga kwa Inu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Lolani kuti m'maŵa ndimve za chikondi chanu chosasinthika, chifukwa ndimakhulupirira Inu. Mundisonyeze njira yoti ndiziyendamo, pakuti ndimapereka mtima wanga kwa Inu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Lolani kuti mmawa ubweretse mawu achikondi chanu chosasinthika, pakuti ine ndimadalira Inu. Mundisonyeze njira yoti ndiyendemo, pakuti kwa Inu nditukulira moyo wanga. |
Mundizindikiritse, ndipo ndidzasunga malamulo anu; ndidzawasamalira ndi mtima wanga wonse.
Mundiphunzitse chokonda Inu; popeza Inu ndinu Mulungu wanga; Mzimu wanu ndi wokoma; munditsogolere kuchidikha.
Mundiphunzitse njira yanu, Yehova, munditsogolere panjira yachidikha, chifukwa cha adani anga.
Pakuti mkwiyo wake ukhala kanthawi kokha; koma kuyanja kwake moyo wonse. Kulira kuchezera, koma mamawa kuli kufuula kokondwera.
Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang'ana iwe.
Koma usana Yehova adzalamulira chifundo chake, ndipo usiku nyimbo yake idzakhala ndi ine. Inde pemphero la kwa Mulungu wa moyo wanga.
Yehova, munditsogolere m'chilungamo chanu, chifukwa cha akundizondawo; mulungamitse njira yanu pamaso panga.
Koma ine, ndidzaimbira mphamvu yanu; inde ndidzaimbitsa chifundo chanu mamawa, pakuti Inu mwakhala msanje wanga, ndi pothawirapo ine tsiku la nsautso yanga.
Mutikhutitse nacho chifundo chanu m'mawa; ndipo tidzafuula mokondwera ndi kukondwera masiku athu onse.
ndipo makutu ako adzamva mau kumbuyo kwa iwe akuti, Njira ndi iyi, yendani inu m'menemo: potembenukira inu kulamanja, ndi potembenukira kulamanzere.
Atero Yehova, Mombolo wako, Woyera wa Israele, Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m'njira yoyenera iwe kupitamo.
Tidziwe tsono, tilondole kudziwa Yehova; kutuluka kwake kwakonzekeratu ngati matanda kucha; ndipo adzatidzera ngati mvula, ngati mvula ya masika yakuthirira dziko.
Nati Manowa, Achitike tsopano mau anu; koma makhalidwe ake a mwanayo ndi machitidwe ake adzatani?
Tsono Davide anati, Kodi amuna a ku Keila adzandipereka ine ndi anyamata anga m'dzanja la Saulo? Ndipo Yehova anati, Adzakupereka.