Musandibisire nkhope yanu tsiku la nsautso yanga; munditchereze khutu lanu; tsiku limene ndiitana ine mundiyankhe msanga.
Masalimo 143:7 - Buku Lopatulika Fulumirani ndiyankheni, Yehova; mzimu wanga ukutha. Musandibisire nkhope yanu; ndingafanane nao akutsikira kudzenje. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Fulumirani ndiyankheni, Yehova; mzimu wanga ukutha. Musandibisire nkhope yanu; ndingafanane nao akutsikira kudzenje. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Fulumirani kundiyankha, Inu Chauta. Ndataya mtima kwambiri, musandibisire nkhope yanu, kuti ndingafanefane ndi anthu otsikira ku manda. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova ndiyankheni msanga; mzimu wanga ukufowoka. Musandibisire nkhope yanu, mwina ndidzakhala ngati iwo amene atsikira ku dzenje. |
Musandibisire nkhope yanu tsiku la nsautso yanga; munditchereze khutu lanu; tsiku limene ndiitana ine mundiyankhe msanga.
Pakuti sanapeputse ndipo sananyansidwe ndi zunzo la wozunzika; ndipo sanambisire nkhope yake; koma pomfuulira Iye, anamva.
Musandibisire ine nkhope yanu; musachotse kapolo wanu ndi kukwiya. Inu munakhala thandizo langa; musanditaye, ndipo musandisiye Mulungu wa chipulumutso changa.
Kwa Inu, Yehova, ndidzafuulira; thanthwe langa, musandikhalire ngati wosamva; pakuti ngati munditontholera ine, ndidzafanana nao iwo akutsikira kumanda.
Ndipo ine ndine wozunzika ndi waumphawi; koma Ambuye andikumbukira ine. Inu ndinu mthandizi wanga, ndi Mpulumutsi wanga, musamachedwa, Mulungu wanga.
Ndalema ndi kufuula kwanga; kum'mero kwauma gwaa! M'maso mwanga mwada poyembekeza Mulungu wanga.
Koma ine ndine wozunzika ndi waumphawi; mundifulumirire, Mulungu. Inu ndinu mthandizi wanga ndi Mpulumutsi wanga; musachedwe, Yehova.
Moyo wanga ulakalaka, inde ukomokanso ndi kufuna mabwalo a Yehova; mtima wanga ndi thupi langa zifuulira kwa Mulungu wamoyo.
Chiyembekezo chozengereza chidwalitsa mtima; koma pakufika chifunirocho ndicho mtengo wa moyo.
Pakuti kunsi kwa manda sikungakuyamikeni Inu; imfa singakulemekezeni; Otsikira kudzenje sangaziyembekeze zoona zanu.
Pakuti sindidzatsutsana kunthawi zonse, sindidzakwiya masiku onse; pakuti mzimu udzalefuka pamaso pa Ine, ndi miyoyo imene ndinailenga.
Ndipo ndidzalindira Yehova, amene wabisira a nyumba ya Yakobo nkhope yake, ndipo ndidzamyembekeza Iye.
anthu akukomoka ndi mantha, ndi kuyembekezera zinthu zilinkudza kudziko lapansi; pakuti mphamvu zakumwamba zidzagwedezeka.