Masalimo 143:6 - Buku Lopatulika Nditambalitsira manja anga kwa Inu: Moyo wanga ulira Inu monga dziko lolira mvula. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nditambalitsira manja anga kwa Inu: Moyo wanga ulira Inu monga dziko lolira mvula. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndimatambalitsira manja anga kwa Inu, mtima wanga umamva ludzu lofuna Inu, monga limachitira dziko louma. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndatambalitsa manja anga kwa Inu; moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Inu monga nthaka yowuma. Sela |
Misozi yanga yakhala ngati chakudya changa, usana ndi usiku; pakunena iwo kwa ine dzuwa lonse, Mulungu wako ali kuti?
Tikadaiwala dzina la Mulungu wathu, ndi kutambasulira manja athu kwa mulungu wachilendo;
Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga; ndidzakufunani m'matanda kucha. Moyo wanga ukumva ludzu la kwa Inu, thupi langa lilirira Inu, m'dziko louma ndi lotopetsa, lopanda madzi.
Moyo wanga ulakalaka, inde ukomokanso ndi kufuna mabwalo a Yehova; mtima wanga ndi thupi langa zifuulira kwa Mulungu wamoyo.
Diso langa lapuwala chifukwa cha kuzunzika kwanga: Ndimaitana Inu, Yehova, tsiku lonse; nditambalitsira manja anga kwa Inu.
Ndipo Mose ananena naye, Potuluka m'mzinda ine, ndidzakweza manja anga kwa Yehova; mabingu adzaleka, ndi matalala sadzakhalaponso; kuti mudziwe kuti dziko lapansi nla Yehova.
Ndipo mchenga wong'azimira udzasanduka thamanda, ndi nthaka yopanda madzi idzasanduka zitsime zamadzi; m'malo a ankhandwe m'mene iwo anagona, mudzakhala udzu ndi mabango ndi milulu.
Koma tsiku lomaliza, lalikululo la chikondwerero, Yesu anaimirira nafuula, ndi kunena, Ngati pali munthu akumva ludzu, adze kwa Ine, namwe.