Masalimo 143:11 - Buku Lopatulika Mundipatse moyo, Yehova, chifukwa cha dzina lanu; mwa chilungamo chanu mutulutse moyo wanga m'sautso. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mundipatse moyo, Yehova, chifukwa cha dzina lanu; mwa chilungamo chanu mutulutse moyo wanga m'sautso. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Sungani moyo wanga, Inu Chauta, kuti dzina lanu lilemekezeke. Munditulutse pa mavuto chifukwa cha kulungama kwanu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Sungani moyo wanga Inu Yehova chifukwa cha dzina lanu; mwa chilungamo chanu tulutseni mʼmasautso anga. |
Ndingakhale ndiyenda pakati pa nsautso, mudzandipatsa moyo; mudzatambasula dzanja lanu pa mkwiyo wa adani anu, ndipo dzanja lanu lamanja lidzandipulumutsa.
Imvani pemphero langa, Yehova; nditcherere khutu kupemba kwanga; ndiyankheni mwa chikhulupiriko chanu, mwa chilungamo chanu.
Chifukwa cha dzina lanu, Yehova, ndikhululukireni kusakaza kwanga, pakuti ndiko kwakukulu.
Ndakhulupirira Inu, Yehova, ndikhale wopanda manyazi nthawi zonse, mwa chilungamo chanu ndipulumutseni ine.
Ndikwatuleni m'chilungamo chanu, ndi kundilanditsa, nditcherereni khutu lanu ndi kundipulumutsa.
Yehova, ndinamva mbiri yanu ndi mantha; Yehova, tsitsimutsani ntchito yanu pakati pa zaka, pakati pa zaka mudziwitse; pa mkwiyo mukumbukire chifundo.