Masalimo 142:7 - Buku Lopatulika Tulutsani moyo wanga m'ndende, kuti ndiyamike dzina lanu; olungama adzandizinga; pakuti mudzandichitira zokoma. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tulutsani moyo wanga m'ndende, kuti ndiyamike dzina lanu; olungama adzandizinga; pakuti mudzandichitira zokoma. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tulutseni m'ndende kuti ndizitamanda dzina lanu. Anthu anu adzandizungulira, chifukwa Inu mwandichitira zabwino zambiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tulutseni mʼndende yanga kuti nditamande dzina lanu. Ndipo anthu olungama adzandizungulira chifukwa cha zabwino zanu pa ine. |
Mundipatse moyo, Yehova, chifukwa cha dzina lanu; mwa chilungamo chanu mutulutse moyo wanga m'sautso.
ndiye wakuchitira chiweruzo osautsika; ndiye wakupatsa anjala chakudya; Yehova amasula akaidi.
Kuti ndibukitse lemekezo lanu lonse; pa bwalo la mwana wamkazi wa Ziyoni, ndidzakondwera nacho chipulumutso chanu.
Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am'nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m'ndende;
yemweyo Mulungu anamuukitsa, atamasula zowawa za imfa, mwakuti sikunali kotheka kuti Iye agwidwe nayo.
Taonani tiwayesera odala opirirawo; mudamva za chipiriro cha Yobu, ndipo mwaona chitsiriziro cha Ambuye, kuti Ambuye ali wodzala chikondi, ndi wachifundo.