Masalimo 142:6 - Buku Lopatulika Tamverani kufuula kwanga; popeza ndisauka kwambiri; ndilanditseni kwa iwo akundilondola; popeza andipambana. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tamverani kufuula kwanga; popeza ndisauka kwambiri; ndilanditseni kwa iwo akundilondola; popeza andilaka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Imvani kulira kwanga, pakuti ndataya mtima. Pulumutseni kwa ondizunza, chifukwa andiposa mphamvu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mverani kulira kwanga pakuti ndathedwa nzeru; pulumutseni kwa amene akundithamangitsa pakuti ndi amphamvu kuposa ine. |
Pakuti mdani alondola moyo wanga; apondereza pansi moyo wanga; andikhalitsa mumdima monga iwo adafa kale lomwe.
Fulumirani ndiyankheni, Yehova; mzimu wanga ukutha. Musandibisire nkhope yanu; ndingafanane nao akutsikira kudzenje.
Yehova, imvani chilungamo, mverani mfuu wanga; tcherani khutu ku pemphero langa losatuluka m'milomo ya chinyengo.
Anandipulumutsa ine kwa mdani wanga wamphamvu, ndi kwa iwo ondida ine, pakuti anandiposa mphamvu.
Ndikadapanda kukhulupirira kuti ndikaone ubwino wa Yehova m'dziko la amoyo, ndikadatani!
Koma adani anga ali ndi moyo, nakhala ndi mphamvu, ndipo akundida kopanda chifukwa achuluka.
Chifukwa chake sitidzachita mantha, lingakhale lisandulika dziko lapansi, angakhale mapiri asunthika, nakhala m'kati mwa nyanja.
Pakuti onani, alalira moyo wanga; amphamvu andipangira chiwembu, osachimwa, osalakwa ine, Yehova,
Musakumbukire motitsutsa mphulupulu za makolo athu; nsoni zokoma zanu zitipeze msanga, pakuti tafooka kwambiri.
Ndidzati kwa Yehova, Pothawirapo panga ndi linga langa; Mulungu wanga, amene ndimkhulupirira.
Nanga mfumu ya Israele inatulukira yani; inu mulikupirikitsa yani? Galu wakufa, kapena nsabwe.