Masalimo 141:9 - Buku Lopatulika Mundisunge ndisagwe mumsampha ananditcherawo, ndisakodwe m'makwekwe a iwo ochita zopanda pake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mundisunge ndisagwe mumsampha ananditcherawo, ndisakodwe m'makwekwe a iwo ochita zopanda pake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mundipulumutse ku msampha umene iwo anditchera, ndi ku makhwekhwe a anthu ochita zoipa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mundipulumutse ku misampha imene anditchera, ku makhwekhwe amene anthu oyipa andikonzera. |
Odzikuza ananditchera msampha, nandibisira zingwe; anatcha ukonde m'mphepete mwa njira; ananditchera makwekwe.
Pamene mzimu wanga unakomoka m'kati mwanga, munadziwa njira yanga. M'njira ndiyendamo ananditchera msampha.
Penyani kudzanja lamanja ndipo muone; palibe wondidziwa; pothawirapo pandisowa; palibe mmodzi wosamalira moyo wanga.
Ndipo anditchera misampha iwo akufuna moyo wanga; ndipo iwo akuyesa kundichitira choipa alankhula zoononga, nalingirira zonyenga tsiku lonse.
Mtima wanga wakhazikika, Mulungu, ndakhazika mtima; ndidzaimba, inde, ndidzaimba zolemekeza.
Mfuu umvekedwe m'nyumba zao, pamene muwatengera khamu la nkhondo dzidzidzi; pakuti akumba dzenje lakundigwira ine, anabisira mapazi anga misampha.
Ndipo anamyang'anira, natumiza ozonda, amene anadzionetsera ngati olungama mtima, kuti akamkole pa mau ake, kotero kuti akampereke Iye ku ukulu ndi ulamuliro wa kazembe.