Mulungu wathu, simudzawaweruza? Pakuti mwa ife mulibe mphamvu yakulimbana nao aunyinji ambiri awa akutidzera; ndipo sitidziwa ngati tidzatani, koma maso athu ali kwa Inu.
Masalimo 141:8 - Buku Lopatulika Pakuti maso anga apenya kwanu, Yehova Ambuye; ndithawira kwa Inu; musataye moyo wanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti maso anga apenya kwanu, Yehova Ambuye; ndithawira kwa Inu; musataye moyo wanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma maso anga amayang'anirabe kwa Inu, Chauta Mulungu wanga. Ndimathaŵira kwa Inu kuti munditeteze, musandisiye opanda wonditchinjiriza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma maso anga akupenyetsetsa Inu Ambuye Wamphamvuzonse; ndimathawira kwa Inu, musandipereke ku imfa. |
Mulungu wathu, simudzawaweruza? Pakuti mwa ife mulibe mphamvu yakulimbana nao aunyinji ambiri awa akutidzera; ndipo sitidziwa ngati tidzatani, koma maso athu ali kwa Inu.
Ndakhulupirira Yehova, mutani nkunena kwa moyo wanga, Thawirani kuphiri lanu ngati mbalame?
Mpsompsoneni Mwanayo, kuti angakwiye, ndipo mungatayike m'njira ukayaka pang'ono pokha mkwiyo wake. Odala onse akumkhulupirira Iye.
Wosauka ndi wosowa afuna madzi, ndipo palibe, ndi lilime lao lilephera, chifukwa cha ludzu; Ine Yehova ndidzawayankha, Ine Mulungu wa Israele sindidzawasiya.