Oipa agwe pamodzi m'maukonde ao, kufikira nditapitirira ine.
Anthu oipa akodwe pamodzi mu ukonde wao womwe, koma ine ndipulumuke.
Anthu oyipa akodwe mʼmaukonde awo, mpaka ine nditadutsa mwamtendere.
Nampachika Hamani pa mtengo adaukonzera Mordekai. Pamenepo mkwiyo wa mfumu unatsika.
Kunena za mutu wao wa iwo akundizinga, choipa cha milomo yao chiwaphimbe.
Chimgwere modzidzimutsa chionongeko; ndipo ukonde wake umene anautcha umkole yekha mwini, agwemo, naonongeke m'mwemo.
Wolungama apulumuka kuvuto; woipa nalowa m'malo mwake.