Masalimo 140:6 - Buku Lopatulika Ndinati kwa Yehova, Inu ndinu Mulungu wanga; munditcherere khutu mau a kupemba kwanga, Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndinati kwa Yehova, Inu ndinu Mulungu wanga; munditcherere khutu mau a kupemba kwanga, Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndimauza Chauta kuti, “Inu ndinu Mulungu wanga,” tcherani khutu kuti mumve liwu la kupemba kwanga, Inu Chauta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu Yehova, ine ndikuti, “Ndinu Mulungu wanga.” Imvani kupempha kwanga Yehova. |
Penyani kudzanja lamanja ndipo muone; palibe wondidziwa; pothawirapo pandisowa; palibe mmodzi wosamalira moyo wanga.
Ndinafuulira kwa inu, Yehova; ndinati, Inu ndinu pothawirapo panga, gawo langa m'dziko la amoyo.
Imvani pemphero langa, Yehova; nditcherere khutu kupemba kwanga; ndiyankheni mwa chikhulupiriko chanu, mwa chilungamo chanu.
Mtima wanga wakhazikika, Mulungu, ndakhazika mtima; ndidzaimba, inde, ndidzaimba zolemekeza.
Ndidzati kwa Yehova, Pothawirapo panga ndi linga langa; Mulungu wanga, amene ndimkhulupirira.
Mfuu umvekedwe m'nyumba zao, pamene muwatengera khamu la nkhondo dzidzidzi; pakuti akumba dzenje lakundigwira ine, anabisira mapazi anga misampha.
Ndi gawo lachitatulo ndidzalitengera kumoto, ndi kuwayenga ngati ayenga siliva, ndi kuwayesa monga ayesa golide; adzaitana dzina langa, ndipo ndidzawamvera; ndidzati, Awa ndi anthu anga; ndi iwo adzati, Yehova ndi Mulungu wanga.