Masalimo 140:13 - Buku Lopatulika Indedi, olungama adzayamika dzina lanu; oongoka mtima adzakhala pamaso panu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Indedi, olungama adzayamika dzina lanu; oongoka mtima adzakhala pamaso panu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zoonadi, anthu ochita zabwino adzatamanda dzina lanu. Anthu amenewo adzakhala pamaso panu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zoonadi anthu olungama adzatamanda dzina lanu, ndipo anthu owongoka mtima adzakhala pamaso panu. |
Mudzandidziwitsa njira ya moyo, pankhope panu pali chimwemwe chokwanira; m'dzanja lanu lamanja muli zokondweretsa zomka muyaya.
Inde ukoma ndi chifundo zidzanditsata masiku onse a moyo wanga, ndipo ndidzakhala m'nyumba ya Yehova masiku onse.
Sekerani mwa Yehova, ndimo kondwerani inu olungama mtima; ndipo fuulani mokondwera nonsenu oongoka mtima.
Mafupa anga onse adzanena, Yehova, afanana ndi Inu ndani, wakulanditsa wozunzika kwa iye amene amposa mphamvu, ndi wozunzika ndi waumphawi kwa iye amfunkhira?
Nenani za wolungama, kuti kudzamkomera iye; chifukwa oterowo adzadya zipatso za machitidwe ao.
Ndipo ngati ndipita kukakonzera inu malo, ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa Ine ndekha; kuti kumene kuli Ineko, mukakhale inunso.
Atate, amene mwandipatsa Ine, ndifuna kuti, kumene ndili Ine, iwonso akhale pamodzi ndi Ine; kuti ayang'anire ulemerero wanga, umene mwandipatsa Ine; pakuti munandikonda Ine lisanakhazikike dziko lapansi.
pamenepo ife okhala ndi moyo, otsalafe, tidzakwatulidwa nao pamodzi m'mitambo, kukakomana ndi Ambuye mumlengalenga, ndipo potero tidzakhala ndi Ambuye nthawi zonse.