Masalimo 140:12 - Buku Lopatulika Ndidziwa kuti Yehova adzanenera wozunzika mlandu, ndi kuweruzira aumphawi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndidziwa kuti Yehova adzanenera wozunzika mlandu, ndi kuweruzira aumphawi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndimadziŵa kuti Inu Chauta mumateteza ozunzika, mumaweruza mwachilungamo anthu osoŵa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndikudziwa kuti Yehova amapereka chiweruzo cholungama kwa anthu osauka, ndipo amateteza zolinga za anthu osowa. |
pamenepo mverani Inu pemphero ndi pembedzero lao mu Mwamba mokhala Inumo, ndi kulimbitsa mlandu wao,
amene amati, Ndi lilime lathu tidzaposa; milomo yathu nja ife eni; mbuye wa pa ife ndani?
Pakuti sanapeputse ndipo sananyansidwe ndi zunzo la wozunzika; ndipo sanambisire nkhope yake; koma pomfuulira Iye, anamva.
Mafupa anga onse adzanena, Yehova, afanana ndi Inu ndani, wakulanditsa wozunzika kwa iye amene amposa mphamvu, ndi wozunzika ndi waumphawi kwa iye amfunkhira?
koma ndi chilungamo adzaweruza aumphawi, nadzadzudzulira ofatsa a m'dziko moongoka; ndipo adzamenya dziko lapansi ndi chibonga cha kukamwa kwake, nadzapha oipa ndi mpweya wa milomo yake.
Iye anaweruza mlandu wa aumphawi ndi osowa; kumeneko kunali kwabwino. Kodi kumeneko si kundidziwa Ine? Ati Yehova.
akhungu alandira kuona kwao, ndi opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, ndi ogontha akumva, ndi akufa aukitsidwa, ndi kwa aumphawi ulalikidwa Uthenga Wabwino.