Ndipo Yehova anavumbitsa pa Sodomu ndi pa Gomora miyala ya sulufure ndi moto kutuluka kwa Mulungu kumwamba;
Masalimo 140:10 - Buku Lopatulika Makala amoto awagwere; aponyedwe kumoto; m'maenje ozama, kuti asaukenso. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Makala amoto awagwere; aponyedwe kumoto; m'maenje ozama, kuti asaukenso. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Makala amoto aŵagwere, aponyedwe m'maenje ozama, asatulukemonso. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Makala amoto agwere pa iwo; aponyedwe pa moto, mʼmaenje amatope, asatulukemonso. |
Ndipo Yehova anavumbitsa pa Sodomu ndi pa Gomora miyala ya sulufure ndi moto kutuluka kwa Mulungu kumwamba;
Adzagwetsa pwatapwata misampha pa oipa; moto ndi miyala ya sulufure, ndi mphepo yoopsa zidzawagawikira m'chikho chao.
Mudzawaika ngati ng'anjo yamoto pa nyengo ya mkwiyo wanu. Yehova adzawatha m'kukwiya kwake, ndipo moto udzawanyeketsa.
Koma Inu, Mulungu, mudzawatsitsira kudzenje la chionongeko. Anthu okhetsa mwazi ndi achinyengo masiku ao sadzafikira nusu; koma ine ndidzakhulupirira Inu.
Ndipo anthu onse adzachita mantha; nadzabukitsa chochita Mulungu, nadzasamalira ntchito yake.
Ndidzayamika Yehova monga mwa chilungamo chake; ndipo ndidzaimbira Yehova Wam'mwambamwamba.
Wosocheretsa oongoka mtima alowe m'njira yoipa, adzagwa mwini m'dzenje lake; koma angwiro adzalandira cholowa chabwino.
Koma amantha, ndi osakhulupirira, ndi onyansa, ndi ambanda, ndi achigololo, ndi olambira mafano, ndi onse a mabodza, cholandira chao chidzakhala m'nyanja yotentha ndi moto ndi sulufure; ndiyo imfa yachiwiri.