Munthu wamlomo sadzakhazikika padziko lapansi; choipa chidzamsaka munthu wachiwawa kuti chimgwetse.
Masalimo 140:1 - Buku Lopatulika Ndilanditseni, Yehova, kwa munthu woipa; ndisungeni kwa munthu wachiwawa; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndilanditseni, Yehova, kwa munthu woipa; ndisungeni kwa munthu wachiwawa; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pulumutseni, Inu Chauta, kwa anthu oipa. Tchinjirizeni kwa anthu ankhanza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Landitseni Yehova kwa anthu oyipa; tetezeni kwa anthu ankhanza, |
Munthu wamlomo sadzakhazikika padziko lapansi; choipa chidzamsaka munthu wachiwawa kuti chimgwetse.
Ndilindireni Yehova, ndisalowe m'manja mwa woipa; ndisungeni kwa munthu wachiwawa; kwa iwo akuti akankhe mapazi anga.
Ukani Yehova, Mumtsekereze, mumgwetse, landitsani moyo wanga kwa woipa ndi lupanga lanu;
Andipulumutsa kwa adani anga. Inde mundikweza pa iwo akundiukira ine, mundikwatula kwa munthu wachiwawa.
Mundiweruzire, Mulungu, ndipo mundinenere mlandu kwa anthu opanda chifundo. Mundilanditse kwa munthu wonyenga ndi wosalungama.
Ndilanditseni, Mulungu wanga, m'dzanja la woipa, m'dzanja la munthu wosalungama ndi wachiwawa.