Masalimo 14:7 - Buku Lopatulika Mwenzi chipulumutso cha Israele chitachokera ku Ziyoni! Pakubweretsa Yehova anthu ake a m'nsinga, pamenepo adzakondwera Yakobo, nadzasekera Israele. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mwenzi chipulumutso cha Israele chitachokera ku Ziyoni! Pakubweretsa Yehova anthu ake a m'nsinga, pamenepo adzakondwera Yakobo, nadzasekera Israele. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chibwere ndithu chipulumutso cha Israele kuchokera ku Ziyoni. Chauta akadzaŵabwezera ufulu anthu ake, Yakobe adzakondwera, Israele adzasangalala kwambiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndithu, chipulumutso cha Israeli chidzachokera ku Ziyoni! Pamene Yehova abwezeretsa ufulu wa anthu ake, Yakobo akondwere ndipo Israeli asangalale! |
Ha, chipulumutso cha Israele chichokere mu Ziyoni! Pakubweretsa Mulungu anthu ake a m'ndende, Yakobo adzakondwera, Israele adzasekera.
ndipo oomboledwa a Yehova adzabwera, nadzafika ku Ziyoni alikuimba; kukondwa kosatha kudzakhala pa mitu yao; iwo adzakhala ndi kusekerera ndi kukondwa, ndipo chisoni ndi kuusa moyo kudzachoka.