Taonani, awa ndi malekezero a njira zake; ndi chimene tikumva za Iye ndi chinong'onezo chaching'ono; koma kugunda kwa mphamvu yake akuzindikiritsa ndani?
Masalimo 139:6 - Buku Lopatulika Kudziwa ichi kundiposa ndi kundidabwitsa: Kundikhalira patali, sindifikirako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kudziwa ichi kundilaka ndi kundidabwitsa: Kundikhalira patali, sindifikirako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nzeru zimenezi nzopitirira nzeru zanga, nzapamwamba, sindingathe kuzimvetsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nzeru zimenezi ndi zopitirira nzeru zanga, ndi zapamwamba kuti ine ndizipeze. |
Taonani, awa ndi malekezero a njira zake; ndi chimene tikumva za Iye ndi chinong'onezo chaching'ono; koma kugunda kwa mphamvu yake akuzindikiritsa ndani?
Ndani uyu abisa uphungu wosadziwa kanthu? Chifukwa chake ndinafotokozera zimene sindinazizindikire, zondidabwitsa, zosazidziwa ine.
Mudzandiiwala chiiwalire, Yehova, kufikira liti? Mudzandibisira ine nkhope yanu kufikira liti?
Inu, Yehova, Mulungu wanga, zodabwitsa zanu mudazichita nzambiri, ndipo zolingirira zanu za pa ife; palibe wina wozifotokozera Inu; ndikazisimba ndi kuzitchula, zindichulukira kuziwerenga.
Ha! Kuya kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziwa kwake kwa Mulungu! Osasanthulikadi maweruzo ake, ndi njira zake nzosalondoleka!