Masalimo 139:24 - Buku Lopatulika Ndipo mupenye ngati ndili nao mayendedwe oipa, nimunditsogolere panjira yosatha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mupenye ngati ndili nao mayendedwe oipa, nimunditsogolere pa njira yosatha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Muwone ngati ndimatsata njira yoipa iliyonse, ndipo munditsogolere m'njira yanu yamuyaya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Onani ngati muli mayendedwe aliwonse oyipa mwa ine, ndipo munditsogolere mʼnjira yanu yamuyaya. |
Mundiphunzitse chokonda Inu; popeza Inu ndinu Mulungu wanga; Mzimu wanu ndi wokoma; munditsogolere kuchidikha.
Mundimvetse chifundo chanu mamawa; popeza ndikhulupirira Inu: Mundidziwitse njira ndiyendemo; popeza ndikweza moyo wanga kwa Inu.
Mudzandidziwitsa njira ya moyo, pankhope panu pali chimwemwe chokwanira; m'dzanja lanu lamanja muli zokondweretsa zomka muyaya.
Mwayesera mtima wanga; mwandizonda usiku; mwandisuntha, simupeza kanthu; mwatsimikiza mtima kuti m'kamwa mwanga simudzalakwa.
Mundiphunzitse njira yanu, Yehova, munditsogolere panjira yachidikha, chifukwa cha adani anga.
Yehova, munditsogolere m'chilungamo chanu, chifukwa cha akundizondawo; mulungamitse njira yanu pamaso panga.
Pakuti chipata chili chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali owerengeka.
Yesu ananena naye, Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.