Masalimo 139:18 - Buku Lopatulika Ndikaziwerenga zichuluka koposa mchenga: Ndikauka ndikhalanso nanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndikaziwerenga zichuluka koposa mchenga: Ndikauka ndikhalanso nanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndikadaŵaŵerenga, bwenzi ali ambiri koposa mchenga. Ndikamadzuka ndimakhala nanube. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndikanaziwerenga, zikanakhala zochuluka kuposa mchenga; pamene ndadzuka, ndili nanube. |
Koma ine ndidzapenyerera nkhope yanu m'chilungamo, ndidzakhuta mtima ndi maonekedwe anu, pamene ndidzauka.
Pakuti zoipa zosawerengeka zandizinga, zochimwa zanga zandipeza kotero kuti sindikhoza kupenya; ziposa tsitsi la mutu wanga, ndipo wandichokera mtima.
Inu, Yehova, Mulungu wanga, zodabwitsa zanu mudazichita nzambiri, ndipo zolingirira zanu za pa ife; palibe wina wozifotokozera Inu; ndikazisimba ndi kuzitchula, zindichulukira kuziwerenga.
Nsembe ndi chopereka simukondwera nazo; mwanditsegula makutu. Nsembe yopsereza ndi yamachimo simunapemphe.
Akufa anu adzakhala ndi moyo; mitembo yao idzauka. Ukani muimbe, inu amene mukhala m'fumbi; chifukwa mame ako akunga mame a pamasamba, ndipo dziko lapansi lidzatulutsa mizimu.
Ndipo ambiri a iwo ogona m'fumbi lapansi adzauka, ena kunka kumoyo wosatha, ndi ena kumanyazi ndi mnyozo wosatha.
amene anafa m'malo mwathu, kuti, tingakhale tidikira, tingakhale tigona, tikakhale ndi moyo pamodzi ndi Iye.