Kodi Iye amene anandilenga ine m'mimba sanamlenge iyenso? Sindiye mmodzi anatiumba m'mimba?
Masalimo 139:13 - Buku Lopatulika Pakuti Inu munalenga impso zanga; munandiumba ndisanabadwe ine. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti Inu munalenga impso zanga; munandiumba ndisanabadwe ine. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti Inu munalenga za mʼkati mwanga; munandiwumba pamodzi mʼmimba mwa amayi anga. |
Kodi Iye amene anandilenga ine m'mimba sanamlenge iyenso? Sindiye mmodzi anatiumba m'mimba?
Inu munandigwiriziza kuyambira ndisanabadwe, kuyambira pa thupi la mai wanga wondichitira zokoma ndinu; ndidzakulemekezani kosalekeza.
atero Yehova, amene anakutenga iwe, nakuumba kuchokera m'mimba, amene adzathangata iwe. Usaope Yakobo, mtumiki wanga ndi iwe, Yesuruni, amene ndakusankha iwe.
Mverani Ine, banja la Yakobo, ndi otsala onse a banja la Israele, amene ndakunyamulani kuyambira m'mimba, ndi kukusenzani chibadwire;
Ndisanakulenge iwe m'mimba ndinakudziwa, ndipo usanabadwe ndinakupatula iwe; ndinakuika kuti ukhale mneneri wa mitundu ya anthu.