Masalimo 137:4 - Buku Lopatulika Tidati, Tidzaimba bwanji nyimbo ya Yehova m'dziko lachilendo? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tidati, Tidzaimba bwanji nyimbo ya Yehova m'dziko lachilendo? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono ife tidati, “Tingaimbe bwanji nyimbo ya Chauta kuchilendo ngati kuno?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tingayimbe bwanji nyimbo za Yehova mʼdziko lachilendo? |
Ndipo tsiku limenelo Ambuye, Yehova wa makamu, anaitana kulira, ndi kugwa misozi, ndi kumeta, ndi kuvala chiguduli m'chuuno;
Pamenepo udzati m'mtima mwako, Ndani wandibalitsa ine amenewa, popeza ana anga anachotsedwa kwa ine, ndipo ndili wouma, ndi wochotsedwa m'dziko, ndi woyendayenda kwina ndi kwina? Ndipo ndani wadza ndi awa? Taona ndinasiyidwa ndekha, amenewa anali kuti?
Sadzatsanulira Yehova nsembe zavinyo; sizidzamkomera Iye nsembe zao; zidzakhala kwa iwo ngati mkate wa achisoni; onse akudyako adzadetsedwa; pakuti mkate wao udzakhala wa njala yao, uwu sudzalowa m'nyumba ya Yehova.
Koma nyimbo za ku Kachisi zidzasanduka kubuma tsiku ilo, ati Ambuye Yehova; mitembo idzachuluka; adzaitaya paliponse padzakhala zii.