Ndipo Mulungu anapanga zounikira zazikulu ziwiri; chounikira chachikulu chakulamulira usana, chounikira chaching'ono chakulamulira usiku, ndi nyenyezi zomwe.
Masalimo 136:9 - Buku Lopatulika Mwezi ndi nyenyezi ziweruze usiku; pakuti chifundo chake nchosatha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mwezi ndi nyenyezi ziweruze usiku; pakuti chifundo chake nchosatha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mwezi ndi nyenyezi kuti zizilamulira usiku, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwezi ndi nyenyezi zilamulire usiku, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya. |
Ndipo Mulungu anapanga zounikira zazikulu ziwiri; chounikira chachikulu chakulamulira usana, chounikira chaching'ono chakulamulira usiku, ndi nyenyezi zomwe.
Pakuona ine thambo la kumwamba lanu, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi, zimene munazikhazika,
Yehova atero, amene apatsa dzuwa kuti liunikire usana, ndi malemba a mwezi ndi a nyenyezi kuti aunikire usiku, amene atonthoza nyanja, pamene mafunde ake agavira; Yehova wa makamu ndi dzina lake: