Ndipo Mulungu anapanga zounikira zazikulu ziwiri; chounikira chachikulu chakulamulira usana, chounikira chaching'ono chakulamulira usiku, ndi nyenyezi zomwe.
Masalimo 136:8 - Buku Lopatulika Dzuwa liweruze usana; pakuti chifundo chake nchosatha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Dzuwa liweruze usana; pakuti chifundo chake nchosatha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Dzuŵa kuti lizilamulira usana, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Dzuwa lilamulire usana, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya. |
Ndipo Mulungu anapanga zounikira zazikulu ziwiri; chounikira chachikulu chakulamulira usana, chounikira chaching'ono chakulamulira usiku, ndi nyenyezi zomwe.
Yehova atero, amene apatsa dzuwa kuti liunikire usana, ndi malemba a mwezi ndi a nyenyezi kuti aunikire usiku, amene atonthoza nyanja, pamene mafunde ake agavira; Yehova wa makamu ndi dzina lake:
kotero kuti mukakhale ana a Atate wanu wa Kumwamba; chifukwa Iye amakwezera dzuwa lake pa oipa ndi pa abwino, namavumbitsira mvula pa olungama ndi pa osalungama.