Ndipo anati Mulungu, Madzi a pansi pakumwamba asonkhane pamodzi pamalo amodzi, uoneke mtunda: ndipo kunatero.
Masalimo 136:6 - Buku Lopatulika Amene anayala dziko lapansi pamwamba pamadzi; pakuti chifundo chake nchosatha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Amene anayala dziko lapansi pamwamba pa madzi; pakuti chifundo chake nchosatha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adayala dziko lapansi pa madzi, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Amene anayala dziko lapansi pamwamba pa madzi, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya. |
Ndipo anati Mulungu, Madzi a pansi pakumwamba asonkhane pamodzi pamalo amodzi, uoneke mtunda: ndipo kunatero.
Ndi Iye amene akhala pamwamba pa malekezero a dziko lapansi, ndipo okhalamo akunga ziwala; amene afutukula thambo ngati chinsalu, naliyala monga hema wakukhalamo;
Atero Mulungu Yehova, Iye amene analenga thambo, nalifutukula, nayala ponse dziko lapansi, ndi chimene chituluka m'menemo, Iye amene amapatsa anthu a m'menemo mpweya, ndi mzimu kwa iwo amene ayenda m'menemo;
Atero Yehova, Mombolo wako, ndi Iye amene anakuumba iwe m'mimba, Ine ndine Yehova, amene ndipanga zinthu zonse, ndi kufunyulula ndekha zakumwamba, ndi kuyala dziko lapansi; ndani ali ndi Ine?
Iye analenga dziko lapansi ndi mphamvu yake, nakhazikitsa dziko lapansi ndi nzeru yake, nayala thambo ndi kuzindikira kwake;
Katundu wa mau a Yehova wakunena Israele. Atero Yehova, wakuyala miyamba, ndi kuika maziko a dziko lapansi, ndi kulenga mzimu wa munthu m'kati mwake;