Masalimo 136:5 - Buku Lopatulika Amene analenga zakumwamba mwanzeru; pakuti chifundo chake nchosatha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Amene analenga zakumwamba mwanzeru; pakuti chifundo chake nchosatha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adalenga zakumwamba ndi nzeru zake, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Amene mwachidziwitso chake anapanga mayiko akumwamba, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya. |
Ndipo Mulungu anapanga thambo, nalekanitsa madzi anali pansi pathambolo ndi madzi anali pamwamba pathambolo; ndipo kunatero.
Ndipo Mulungu analitcha thambolo Kumwamba. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachiwiri.
Ntchito zanu zichulukadi, Yehova! Munazichita zonse mwanzeru; dziko lapansi lidzala nacho chuma chanu.
Zakumwamba zinalengedwa ndi mau a Yehova; ndipo ndi mpweya wa m'kamwa mwake khamu lao lonse.
Iye analenga dziko lapansi ndi mphamvu yake, nakhazikitsa dziko lapansi ndi nzeru yake, nayala thambo ndi kuzindikira kwake;
Iye analenga dziko lapansi ndi mphamvu yake, wakhazika dziko lapansi ndi nzeru yake, ndi luso anayala thambo;