Masalimo 136:4 - Buku Lopatulika Amene yekha achita zodabwitsa zazikulu; pakuti chifundo chake nchosatha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Amene yekha achita zodabwitsa zazikulu; pakuti chifundo chake nchosatha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta yekhayo amachita zodabwitsa zazikulu, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye yekhayo amene amachita zodabwitsa zazikulu, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya. |
Afanana ndi Inu ndani mwa milungu, Yehova? Afanana ndi Inu ndani, wolemekezedwa, woyera, woopsa pomyamika, wakuchita zozizwa?
Ndipo aimba nyimbo ya Mose kapolo wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa, nanena, Ntchito zanu nzazikulu ndi zozizwitsa, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse; njira zanu nzolungama ndi zoona, Mfumu Inu ya nthawi zosatha.