Masalimo 136:10 - Buku Lopatulika Iye amene anapandira Aejipito ana ao oyamba; pakuti chifundo chake nchosatha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Iye amene anapandira Aejipito ana ao oyamba; pakuti chifundo chake nchosatha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adapha ana achisamba a ku Ejipito, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Amene anakantha ana woyamba kubadwa a Igupto, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya. |
Pakuti ndidzapita pakati padziko la Ejipito usiku womwewo, ndi kukantha ana oyamba onse m'dziko la Ejipito, anthu ndi zoweta; ndipo ndidzachita maweruzo pa milungu yonse ya Aejipito; Ine ndine Yehova.
Ndipo panakhala pakati pa usiku, Yehova anakantha ana oyamba onse a m'dziko la Ejipito, kuyambira mwana woyamba wa Farao wakukhala pa mpando wachifumu wake kufikira mwana woyamba wa wam'nsinga ali m'kaidi; ndi ana oyamba onse a zoweta.
Ndipo mtundu umene udzawayesa akapolo, ndidzauweruza Ine, anatero Mulungu; ndipo zitapita izi adzatuluka, nadzanditumikira Ine m'malo muno.
Ndi chikhulupiriro anachita Paska, ndi kuwaza kwa mwazi, kuti wakuononga ana oyamba angawakhudze iwo.