Pakuti Davide anati, Yehova Mulungu wa Israele wapumulitsa anthu ake; ndipo akhala mu Yerusalemu kosatha;
Masalimo 135:21 - Buku Lopatulika Alemekezedwe Yehova kuchokera mu Ziyoni, amene akhala mu Yerusalemu. Aleluya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Alemekezedwe Yehova kuchokera m'Ziyoni, amene akhala m'Yerusalemu. Aleluya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Atamandike ku Ziyoni Chauta, amene amakhala ku Yerusalemu! Tamandani Chauta! Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Wodalitsika ndi Yehova kuchokera mʼZiyoni, amene amakhala mu Yerusalemu. Tamandani Yehova. |
Pakuti Davide anati, Yehova Mulungu wa Israele wapumulitsa anthu ake; ndipo akhala mu Yerusalemu kosatha;
Koma ndinasankha Yerusalemu, kuti dzina langa likhale komweko; ndinasankhanso Davide akhale mfumu ya anthu anga Israele.
pamodzi ndi siliva ndi golide zilizonse ukazipeza m'dziko lonse la ku Babiloni, pamodzi ndi chopereka chaufulu cha anthu, ndi cha ansembe, akuperekera mwaufulu nyumba ya Mulungu wao ili ku Yerusalemu;
Yehova adzakudalitsa ali mu Ziyoni; ndipo udzaona zokoma za Yerusalemu masiku onse a moyo wako.
Yehova ndiye wamkulu, ayenera kulemekezekadi, m'mzinda wa Mulungu wathu, m'phiri lake loyera.
Phiri la Ziyoni, chikhalidwe chake nchokoma kumbali zake za kumpoto, ndilo chimwemwe cha dziko lonse lapansi, mzinda wa mfumu yaikulu.
Tafuula, takuwa iwe, wokhala mu Ziyoni, chifukwa Woyera wa Israele wa m'kati mwako ali wamkulu.
Sayang'anira mphulupulu ili mu Yakobo, kapena sapenya kupulukira kuli mu Israele. Yehova Mulungu wake ali ndi iye, ndi mfuu wa mfumu uli pakati pao.