Ndipo Davide anati kwa khamu lonse, Mulemekeze tsono Yehova Mulungu wanu. Ndi khamu lonse linalemekeza Yehova Mulungu wa makolo ao, nawerama, nalambira Yehova, ndi mfumu.
Masalimo 135:19 - Buku Lopatulika A nyumba ya Israele inu, lemekezani Yehova: A nyumba ya Aroni inu, lemekezani Yehova: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 A nyumba ya Israele inu, lemekezani Yehova: A nyumba ya Aroni inu, lemekezani Yehova: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu a m'banja la Israele, tamandani Chauta! Inu a m'banja la Aroni, tamandani Chauta! Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu nyumba ya Israeli, tamandani Yehova; inu nyumba ya Aaroni, tamandani Yehova; |
Ndipo Davide anati kwa khamu lonse, Mulemekeze tsono Yehova Mulungu wanu. Ndi khamu lonse linalemekeza Yehova Mulungu wa makolo ao, nawerama, nalambira Yehova, ndi mfumu.
Yehova watikumbukira; adzatidalitsa: adzadalitsa nyumba ya Israele; adzadalitsa nyumba ya Aroni.
Ndipo anakweza nyanga ya anthu ake, chilemekezo cha okondedwa ake onse; ndiwo ana a Israele, anthu a pafupi pa Iye. Aleluya.
Ndipo mau anachokera kumpando wachifumu, ndi kunena, Lemekezani Mulungu wathu akapolo ake onse akumuopa Iye, aang'ono ndi aakulu.