Masalimo 135:18 - Buku Lopatulika Akuwapanga adzafanana nao; inde, onse akuwakhulupirira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Akuwapanga adzafanana nao; inde, onse akuwakhulupirira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu amene amapanga mafanowo afanefane nawo, chimodzimodzi onse amene amaŵakhulupirira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo amene amapanga mafanowo adzakhala ngati mafanowo, chimodzimodzinso iwo amene amadalira mafanowo. |
Onse akutumikira fano losema, akudzitamandira nao mafano, achite manyazi: Mgwadireni Iye, milungu yonse inu.
Iwo adzabwezedwa m'mbuyo, adzakhala ndi manyazi ambiri amene akhulupirira mafano osemedwa, nati kwa mafano oyengeka, Inu ndinu milungu yathu.
mwa amene mulungu wa nthawi ino ya pansi pano anachititsa khungu maganizo ao a osakhulupirira, kuti chiwalitsiro cha Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Khristu, amene ali chithunzithunzi cha Mulungu, chisawawalire.