polankhula Iye, pali unyinji wa madzi m'mwamba, ndipo akweretsa nkhungu ku malekezero a dziko lapansi, alenga mphezi idzetse mvula, natulutsa mphepo m'zosungira zake.
Masalimo 135:17 - Buku Lopatulika makutu ali nao, koma osamva; inde, pakamwa pao palibe mpweya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 makutu ali nao, koma osamva; inde, pakamwa pao palibe mpweya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Makutu ali nawo, koma saamva, ndipo alibe mpweya m'kamwa mwao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero makutu ali nawo, koma sakumva ndipo mʼkamwa mwawo mulibe mpweya uliwonse. |
polankhula Iye, pali unyinji wa madzi m'mwamba, ndipo akweretsa nkhungu ku malekezero a dziko lapansi, alenga mphezi idzetse mvula, natulutsa mphepo m'zosungira zake.
Anthu onse ali opulukira ndi opanda nzeru; wakusula golide achitidwa manyazi ndi fanizo lake losema; pakuti fanizo lake loyenga lili bodza, mulibe mpweya m'menemo.
Ndipo tsopano aonjeza kuchimwa, nadzipangira mafano oyenga a siliva wao, mafano monga mwa nzeru zao, onsewo ntchito ya amisiri; anena za iwo, Anthu ophera nsembe apsompsone anaang'ombe.
Tsoka iye wakunena kwa mtengo, Galamuka; ndi kwa mwala wosalankhula, Nyamuka! Kodi ichi chiphunzitsa? Taona chakutidwa ndi golide ndi siliva, ndi m'kati mwake mulibe mpweya konse.