Ndipo anaponya milungu yao pamoto; pakuti iyo sinali milungu, koma ntchito yopangidwa ndi manja a anthu, mtengo ndi mwala; chifukwa chake iwo anaiononga.
Masalimo 135:15 - Buku Lopatulika Mafano a amitundu ndiwo siliva ndi golide, ntchito ya manja a anthu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mafano a amitundu ndiwo siliva ndi golide, ntchito ya manja a anthu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mafano a mitundu ina ya anthu ndi asiliva ndi agolide chabe, ndi opangidwa ndi manja a anthu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mafano a mitundu ya anthu ndi siliva ndi golide, opangidwa ndi manja a anthu. |
Ndipo anaponya milungu yao pamoto; pakuti iyo sinali milungu, koma ntchito yopangidwa ndi manja a anthu, mtengo ndi mwala; chifukwa chake iwo anaiononga.
Popeza tsono tili mbadwa za Mulungu, sitiyenera kulingalira kuti umulungu uli wofanafana ndi golide, kapena siliva, kapena mwala, wolocha ndi luso ndi zolingalira za anthu.
Ndipo kumeneko mudzatumikira milungu, ntchito ya manja a anthu, mtengo ndi mwala, yosapenya, kapena kumva, kapena kudya, kapena kununkhiza.