Masalimo 135:13 - Buku Lopatulika Dzina lanu, Yehova, likhala kosatha; chikumbukiro chanu, Yehova, kufikira mibadwomibadwo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Dzina lanu, Yehova, likhala kosatha; chikumbukiro chanu, Yehova, kufikira mibadwomibadwo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Dzina lanu, Inu Chauta, nlamuyaya, kutchuka kwanu ndi kwa pa mibadwo yonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Dzina lanu, Inu Yehova, ndi losatha mpaka muyaya, mbiri yanu, Inu Yehova, idziwika mibado yonse. |
Inu mudzauka, ndi kuchitira nsoni Ziyoni; popeza yafika nyengo yakumchitira chifundo, nyengo yoikika.
Dzina lake lidzakhala kosatha, momwe likhalira dzuwa dzina lake lidzamvekera zidzukulu. Ndipo anthu adzadalitsidwa mwa Iye; amitundu onse adzamutcha wodala.
Yehova, Ambuye wathu, dzina lanu liposadi nanga padziko lonse lapansi! Inu amene munaika ulemerero wanu pa thambo la kumwamba.
Ndidzaimbira zachifundo za Yehova nthawi yonse, pakamwa panga ndidzadziwitsira chikhulupiriko chanu ku mibadwomibadwo.
Ndipo Mulungu ananenanso kwa Mose, Ukatero ndi ana a Israele, Yehova Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo anandituma kwa inu; ili ndi dzina langa nthawi yosatha, ichi ndi chikumbukiro changa m'mibadwomibadwo.
Chifukwa chake pempherani inu chomwechi: Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe.