Akandipanda munthu wolungama ndidzati nchifundo: akandidzudzula, ndidzakuyesa mafuta a pamutu; mutu wanga usakane: Pakuti pangakhale posautsidwa iwo ndidzawapempherera.
Masalimo 133:2 - Buku Lopatulika Ndiko ngati mafuta a mtengo wake pamutu, akutsikira kundevu, inde kundevu za Aroni; akutsikira kumkawo wa zovala zake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndiko ngati mafuta a mtengo wake pamutu, akutsikira kundevu, inde kundevu za Aroni; akutsikira kumkawo wa zovala zake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndi ngati mafuta amtengowapatali oŵathira pa mutu, otsikira ku ndevu, ku ndevu za Aroni, oyenderera mpaka ku khosi la mkanjo wake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zili ngati mafuta amtengowapatali othiridwa pa mutu, otsikira ku ndevu, ku ndevu za Aaroni, oyenderera mpaka mʼkhosi mwa mkanjo wake. |
Akandipanda munthu wolungama ndidzati nchifundo: akandidzudzula, ndidzakuyesa mafuta a pamutu; mutu wanga usakane: Pakuti pangakhale posautsidwa iwo ndidzawapempherera.
Ndipo pa mbinyiru wake upange makangaza a lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, pambinyiru pake pozungulira, ndi kuwapakiza ndi miliu yagolide pozungulira;
ndipo uzikonza nazo chofukiza, chosakaniza mwa machitidwe a wosakaniza, chokometsera ndi mchere, choona, chopatulika;
Napangira pa mkawo wa mwinjiro makangaza a lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.
Mafuta ndi zonunkhira zikondweretsa mtima, ndi ubwino wa bwenzi uteronso pakupangira uphungu.
Mafuta ako anunkhira bwino; dzina lako likunga mafuta onunkhira otsanulidwa; chifukwa chake anamwali akukonda.
Pamenepo Maria m'mene adatenga muyeso umodzi wa mafuta onunkhira bwino a narido weniweni a mtengo wake wapatali, anadzoza mapazi a Yesu, napukuta mapazi ake ndi tsitsi lake; ndipo nyumba inadzazidwa ndi mnunkho wake wa mafutawo.