Ukani, Yehova, lowani ku mpumulo wanu; Inu ndi hema wa mphamvu yanu.
Dzambatukani, Inu Chauta, ndi kupita ku malo anu kumene mumakhala, Inuyo pamodzi ndi bokosi lachipangano lofanizira mphamvu zanu.
‘Dzukani Yehova, ndipo bwerani ku malo anu opumulira, Inuyo ndi Bokosi la Chipangano limene limafanizira mphamvu zanu.
Auke Mulungu, abalalike adani ake; iwonso akumuda athawe pamaso pake.
napereka mphamvu yake mu ukapolo, ndi ulemerero wake m'dzanja la msautsi.