Masalimo 132:7 - Buku Lopatulika Tidzalowa mokhalamo Iye; tidzagwadira kumpando wa mapazi ake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tidzalowa mokhalamo Iye; tidzagwadira kumpando wa mapazi ake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Tiyeni tipite kumalo kumene Chauta amakhala. Tiyeni tikapembedze ku mpando wake wachifumu.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Tiyeni tipite ku malo ake okhalamo; tiyeni tikamulambire pa mapazi ake. |
Koma ine, mwa kuchuluka kwa chifundo chanu ndidzalowa m'nyumba yanu; ndidzagwada kuyang'ana Kachisi wanu woyera ndi kuopa Inu.
Mkwezeni Yehova Mulungu wathu, ndipo gwadirani poponderapo mapazi ake: Iye ndiye Woyera.
Mkwezeni Yehova Mulungu wathu, ndipo gwadirani paphiri lake loyera; pakuti Yehova Mulungu wathu ndiye woyera.
Ndipo anthu ambiri adzanka, nati, Tiyeni tikwere kunka kuphiri la Yehova, kunyumba ya Mulungu wa Yakobo; ndipo Iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m'mayendedwe ake; chifukwa mu Ziyoni mudzatuluka chilamulo, ndi mau a Yehova kuchokera mu Yerusalemu.
Ambuye waphimbatu ndi mtambo mwana wamkazi wa Ziyoni, pomkwiyira! Wagwetsa pansi kuchokera kumwamba kukoma kwake kwa Israele; osakumbukira poponda mapazi ake tsiku la mkwiyo wake.