Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Masalimo 132:5 - Buku Lopatulika

kufikira nditapezera Yehova malo, chokhalamo Wamphamvuyo wa Yakobo?

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

kufikira nditapezera Yehova malo, chokhalamo Wamphamvuyo wa Yakobo?

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

mpaka nditapezera Chauta malo, malo oti Mulungu Wamphamvuzonse wa Yakobe azikhalamo.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

mpaka nditamupezera malo Yehova, malo okhala a Wamphamvu wa Yakobo.”

Onani mutuwo



Masalimo 132:5
12 Mawu Ofanana  

Ndipo pamene adalowa nalo likasa la Mulungu analiika pamalo pake pakati pa hema amene Davide adaliutsira; ndipo Davide anapereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zoyamika pamaso pa Yehova.


Ndipo kunali pakukhala mfumuyo m'nyumba mwake, atampumulitsa Yehova pa adani ake onse omzungulira,


Ndipo Davide atate wanga anafuna m'mtima mwake kumangira dzina la Yehova Mulungu wa Israele nyumba.


Kodi Mulungu adzakhala ndithu padziko lapansi? Taonani, thambo ndi mu Mwambamwamba zichepa kukulandirani, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimangayi.


Inu ndinu akulu a nyumba za makolo a Alevi, mudzipatule inu ndi abale anu omwe, kuti mukatenge ndi kukwera nalo likasa la Yehova Mulungu wa Israele ku malo ndalikonzera.


Ndipo Davide anasonkhanitsira Aisraele onse ku Yerusalemu, akwere nalo likasa la Yehova kumalo kwake adalikonzera.


Ndipo Davide anati kwa Solomoni mwana wake, Kunena za ine, kumtima kwanga kudati, ndilimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba.


Ndipo mfumu Davide anaima chilili, nati, Mundimvere ine, abale anga ndi anthu anga, ine kumtima kwanga ndinafuna kulimangira likasa la chipangano la Yehova, ndi popondapo mapazi a Mulungu wathu nyumba yopumulira, ndipo ndidakonzeratu za nyumbayi.


Koma ali nayo mphamvu ndani yakummangira Iye nyumba, popeza thambo lam'mwambamwamba silimfikira? Ndine yani ine tsono, kuti ndimmangire nyumba, koma kumfukizira chofukiza ndiko?


Atero Yehova, Kumwamba ndi mpando wanga wachifumu, ndi dziko lapansi ndi choikapo mapazi anga; mudzandimangira Ine nyumba yotani? Ndi malo ondiyenera kupumamo ali kuti?


chimene inunso mumangidwamo pamodzi, mukhale chokhalamo Mulungu mwa Mzimu.