Ndipo tsopano nyamukani, Yehova Mulungu, kudza kopumulira kwanu, Inu ndi likasa la mphamvu yanu; ansembe anu, Yehova Mulungu, avale chipulumutso; ndi okondedwa anu akondwere nazo zabwino.
Masalimo 132:16 - Buku Lopatulika Ndipo ansembe ake ndidzawaveka ndi chipulumutso: Ndi okondedwa ake adzafuulitsa mokondwera. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ansembe ake ndidzawaveka ndi chipulumutso: Ndi okondedwa ake adzafuulitsa mokondwera. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ansembe ake ndidzaŵaveka chipulumutso, anthu ake oyera mtima adzafuula ndi chimwemwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndidzaveka ansembe ake chipulumutso, ndipo anthu ake oyera mtima adzayimba nthawi zonse nyimbo zachimwemwe. |
Ndipo tsopano nyamukani, Yehova Mulungu, kudza kopumulira kwanu, Inu ndi likasa la mphamvu yanu; ansembe anu, Yehova Mulungu, avale chipulumutso; ndi okondedwa anu akondwere nazo zabwino.
Ndilindireni Yehova, ndisalowe m'manja mwa woipa; ndisungeni kwa munthu wachiwawa; kwa iwo akuti akankhe mapazi anga.
Ndidzakondwa kwambiri mwa Yehova, moyo wanga udzakondwerera mwa Mulungu wanga; pakuti Iye wandiveka ine ndi zovala za chipulumutso, nandifunda chofunda cha chilungamo, monga mkwati avala nduwira, ndi monga mkwatibwi adzikometsa yekha ndi miyala yamtengo.
Efuremu andizinga ndi bodza, ndi nyumba ya Israele ndi chinyengo, ndi Yuda apikisana ndi Mulungu, ndiye Woyera wokhulupirika.
Kondwera kwambiri, mwana wamkazi wa Ziyoni; fuula mwana wamkazi wa Yerusalemu; taona, Mfumu yako ikudza kwa iwe; ndiye wolungama, ndi mwini chipulumutso; wofatsa ndi wokwera pabulu, ndi mwana wamphongo wa bulu.
Kufikira tsopano simunapemphe kanthu m'dzina langa; pemphani, ndipo mudzalandira, kuti chimwemwe chanu chikwaniridwe.