komatu sindidzachotsa ufumu wonsewo; fuko limodzi ndidzapatsa mwana wako, chifukwa cha Davide mtumiki wanga, ndi chifukwa cha Yerusalemu amene ndinamsankha.
Masalimo 132:13 - Buku Lopatulika pakuti Yehova anasankha Ziyoni; analikhumba likhale pokhala pake; ndi kuti, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 pakuti Yehova anasankha Ziyoni; analikhumba likhale pokhala pake; ndi kuti, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta wasankhula Ziyoni, akufuna kuti akhale malo ake okhalamo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti Yehova wasankha Ziyoni, Iye wakhumba kuti akhale malo ake okhalamo: |
komatu sindidzachotsa ufumu wonsewo; fuko limodzi ndidzapatsa mwana wako, chifukwa cha Davide mtumiki wanga, ndi chifukwa cha Yerusalemu amene ndinamsankha.
Pakuti ndasankha ndi kuipatula nyumba iyi, kuti dzina langa likhaleko chikhalire; inde maso anga ndi mtima wanga zidzakhala komweko kosalekeza.
Aliyense mwa inu a anthu ake onse, Mulungu wake akhale naye, akwere kunka ku Yerusalemu, ndiwo mu Yuda, nakaimange nyumba ya Yehova Mulungu wa Israele; Iye ndiye Mulungu wokhala mu Yerusalemu.
Muchitiranji nsanje mapiri inu a mitumitu, ndi phirilo Mulungu analikhumba, akhaleko? Inde, Yehova adzakhalabe komweko kosatha.
Ndipo adzayankhanji amithenga a amitundu? Kuti Yehova wakhazikitsa Ziyoni, ndipo m'menemo anthu ake ovutidwa adzaona pobisalira.
Komatu mwayandikira kuphiri la Ziyoni, ndi mzinda wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wa Kumwamba, ndi kwa unyinji wochuluka wa angelo,