Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Masalimo 132:10 - Buku Lopatulika

Chifukwa cha Davide mtumiki wanu musabweze nkhope ya wodzozedwa wanu.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Chifukwa cha Davide mtumiki wanu musabweze nkhope ya wodzozedwa wanu.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Chifukwa cha zimene mudalonjeza kwa mtumiki wanu Davide, musakane nkhope ya wodzozedwa wanu.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Chifukwa cha Davide mtumiki wanu, musakane wodzozedwa wanu.

Onani mutuwo



Masalimo 132:10
11 Mawu Ofanana  

Koma sindidzalanda ufumu wonse m'dzanja lake, koma ndidzamkhalitsa mfumu masiku ake onse, chifukwa cha Davide mtumiki wanga amene uja ndinamsankha, chifukwa kuti anasunga malamulo anga ndi malemba anga.


Pakuti ndidzatchinjiriza mzinda uno kuupulumutsa, chifukwa cha Ine mwini, ndi chifukwa cha Davide mtumiki wanga.


Koma Yehova sanafune kuononga Yuda, chifukwa cha Davide mtumiki wake monga adamuuza, kuti adzampatsa nyali ya kwa ana ake kosalekeza.


Yehova Mulungu, musabweza nkhope ya wodzozedwa wanu, mukumbukire zachifundo za Davide mtumiki wanu.


Ndiye amene apatsa mafumu chipulumutso: Amene alanditsa Davide mtumiki wake kulupanga loipa.


Pakuti tsiku limodzi m'mabwalo anu likoma koposa masiku ambirimbiri akukhala pena. Kukhala ine wapakhomo m'nyumba ya Mulungu wanga, kundikonda ine koposa kugonera m'mahema a choipa.


Onani, Mulungu, ndinu chikopa chathu; ndipo penyani pa nkhope ya Wodzozedwa wanu.


atatero ana a Israele adzabwera, nadzafuna Yehova Mulungu wao, ndi Davide mfumu yao, nadzafika ndi mantha kwa Yehova, ndi ku ukoma wake masiku otsiriza.